Masalimo
Nyimbo yotamanda Mulungu. Salimo la Davide.
א [ʼAʹleph]
145 Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+
Ndipo ndidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
ב [Behth]
ג [Giʹmel]
ד [Daʹleth]
ה [Heʼ]
ו [Waw]
6 Anthu adzanena za zochita zanu zamphamvu ndi zochititsa mantha.+
Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.+
ז [Zaʹyin]
7 Iwo adzalankhula mosefukira za kuchuluka kwa ubwino wanu,+
Ndipo adzafuula mokondwera chifukwa cha chilungamo chanu.+
ח [Chehth]
8 Yehova ndi wachisomo ndi wachifundo,+
Wosakwiya msanga ndi wosonyeza kukoma mtima kosatha komanso kwakukulu.+
ט [Tehth]
י [Yohdh]
כ [Kaph]
מ [Mem]
13 Ufumu wanu ndi ufumu umene udzakhalapobe mpaka kalekale.+
Ulamuliro wanu udzakhalapobe ku mibadwo yonse.+
ס [Saʹmekh]
14 Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa,+
Ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.+
ע [ʽAʹyin]
15 Zolengedwa zonse zimayang’ana kwa inu mwachiyembekezo,+
Ndipo mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+
פ [Peʼ]
צ [Tsa·dhehʹ]
ק [Qohph]
18 Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.+
Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi,+
ר [Rehsh]
19 Ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo,+
Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.+
ש [Shin]
ת [Taw]