28“Koma iwe patula Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli, ndipo Aroniyo+ atumikire monga wansembe wanga pamodzi ndi ana akewo,+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+
5 Chimene chichitike n’chakuti, munthu amene ndimusankheyo,+ ndodo yake idzaphuka, ndipo ndidzathetseratu kudandaula+ kwa ana a Isiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine, pamene akudandaula motsutsana nawe.”+