Salimo 34:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.+Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.+ Salimo 51:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi,+Kuti pakamwa panga patamande inu.+ Salimo 71:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+ Salimo 89:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+
8 M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+
89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+