Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. Pa nthawi imene mneneri Natani anapita kwa Davide atagona ndi Bati-seba.+
51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+
Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+
4 Ine ndakuchimwirani kwambiri,+
Ndipo ndachita chinthu choipa pamaso panu,+
Choncho mukamalankhula mumalankhula zachilungamo,+
Ndipo mukamaweruza, mumaweruza molungama.+
5 Taonani! Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa.+
Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+
6 Taonani! Mumakondwera ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.+
Ndipo mundidziwitse nzeru mumtima mwanga.+
7 Ndiyeretseni ndi hisope ku machimo anga kuti ndikhale woyera.+
Ndisambitseni kuti ndiyere kwambiri kuposa chipale chofewa.+
12 Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chifukwa cha chipulumutso chanu,+
Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.+
14 Inu Mulungu, ndilanditseni ku mlandu wa magazi,+ inu Mulungu wa chipulumutso changa,+
Kuti lilime langa linene za chilungamo chanu mokondwera.+
16 Pakuti nsembe singakusangalatseni, chifukwa ikanakusangalatsani ndikanaipereka kwa inu.+
Nsembe yopsereza yathunthu singakusangalatseni.+