Ekisodo 15:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, mlongo wake wa Aroni,+ anatenga maseche m’manja mwake,+ ndipo akazi ena onse anam’tsatira akuimba maseche ndi kuvina.+ Oweruza 11:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa.+ Atafika kumeneko anaona mwana wake wamkazi akubwera kudzam’chingamira, akuimba maseche ndi kuvina.+ Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. Salimo 150:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mutamandeni ndi maseche+ ndi gule wovina mozungulira.+Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+ Yeremiya 31:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 “Pa nthawi imeneyo, namwali, anyamata ndi amuna achikulire, onse pamodzi adzasangalala ndipo adzavina.+ Ndidzawachotsera chisoni chawo, moti kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo ndipo ndidzawatonthoza ndi kuwasangalatsa.+
20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, mlongo wake wa Aroni,+ anatenga maseche m’manja mwake,+ ndipo akazi ena onse anam’tsatira akuimba maseche ndi kuvina.+
34 Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa.+ Atafika kumeneko anaona mwana wake wamkazi akubwera kudzam’chingamira, akuimba maseche ndi kuvina.+ Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
4 Mutamandeni ndi maseche+ ndi gule wovina mozungulira.+Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+
13 “Pa nthawi imeneyo, namwali, anyamata ndi amuna achikulire, onse pamodzi adzasangalala ndipo adzavina.+ Ndidzawachotsera chisoni chawo, moti kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo ndipo ndidzawatonthoza ndi kuwasangalatsa.+