Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 22:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa.+

      Koma mumatsutsa odzikweza, kuti muwatsitse.+

  • Salimo 10:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Chifukwa cha kutukumuka mtima kwake, woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.+

      Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+

  • Salimo 18:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+

      Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+

  • Salimo 101:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+

      Ndimamukhalitsa chete.+

      Sindingathe kupirira zochita za+

      Aliyense wodzikweza ndi wamtima wonyada.+

  • Miyambo 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+

  • Miyambo 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chikwapu cha kudzikuza chili m’kamwa mwa wopusa,+ koma anthu anzeru milomo yawo imawatsogolera.+

  • Yesaya 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+

  • Luka 18:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri+ kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”+

  • 1 Petulo 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chimodzimodzinso inu anyamata. Muzigonjera+ amuna achikulire. Koma nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa,+ chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena