Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati:
18 Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+
2 Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+
Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+
Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+
6 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,
Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+
Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+
Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
7 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+
Maziko a mapiri anagwedezeka,+
Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+
8 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+
Makala onyeka anatuluka mwa iye.
10 Iye anafika atakwera pakerubi wouluka.+
Mulungu anali kuuluka mwaliwiro pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+
11 Kenako anapanga mdima kukhala malo ake obisalamo,+
Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda,
Zimene zinamuzungulira ngati msasa wake.+
12 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka mitambo yake,+
Munatulukanso matalala ndi makala onyeka a moto.+
13 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+
Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake,+
Anatulutsanso matalala ndi makala onyeka a moto.
15 Ndipo ngalande za pansi pa madzi zinaonekera,+
Maziko a dziko lapansi anakhala poonekera.+
Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwanu.+
17 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+
Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+
20 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+
Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+
21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+
Sindinachoke kwa Mulungu wanga. Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.+
24 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+
Andibwezere mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.+
25 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+
Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+
26 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+
Kwa munthu wopotoka maganizo mudzadzisonyeza kuti ndinu wochenjera,+
27 Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+
Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+
29 Pakuti ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba.+
Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+
30 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+
Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+
Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
32 Mulungu woona Ndiye amandilimbitsa,*+
Ndipo adzasalaza njira yanga.+
33 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+
Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+
35 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+
Dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza,+
Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.+
40 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+
Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+
41 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+
Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+
43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+
Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+
Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
44 Anthu akangomva mphekesera chabe zokhudza ine, adzandimvera.+
Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+
46 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+
Mulungu wa chipulumutso changa akhale wokwezeka.+
47 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga.+
Iye amagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika kunsi kwa mapazi anga.+
48 Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.+
Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+
Mudzandilanditsa kwa munthu wachiwawa.+