Ekisodo 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+ 2 Mafumu 6:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Koma Elisa anati: “Musawaphe. Kodi mukufuna kupha anthu amene mwawagonjetsa ndi lupanga ndi uta n’kuwagwira?+ Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa.+ Kenako apite kwa mbuye wawo.” Miyambo 24:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere,+ Mateyu 5:44 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 44 Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+
5 Ukaona bulu wa munthu wodana nawe atagona pansi polemedwa ndi katundu, pamenepo usam’siye yekha munthu wodana naweyo. Uthandizane naye kumasula katunduyo.+
22 Koma Elisa anati: “Musawaphe. Kodi mukufuna kupha anthu amene mwawagonjetsa ndi lupanga ndi uta n’kuwagwira?+ Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa.+ Kenako apite kwa mbuye wawo.”