Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndipo atumiki anu onsewa adzatsika ndi kubwera kwa ine, n’kundigwadira ndi kundiweramira.+ Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’ Zitatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.

  • 1 Mbiri 12:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndiyeno panali Agadi ena amene anasankha kupita kumbali ya Davide m’chipululu,+ kumalo ovuta kufikako. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima, asilikali okonzekera nkhondo, amene zishango zawo zazikulu ndi mikondo yawo ing’onoing’ono zinkakhala zokonzeka.+ Nkhope zawo zinali ngati nkhope za mikango,+ ndipo liwiro lawo linali ngati la mbawala m’mapiri.+

  • Danieli 3:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pamenepo Sadirake, Mesake ndi Abedinego anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu Nebukadinezara, palibenso chimene ife tinganene kwa inu pa nkhani imeneyi.+

  • Machitidwe 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Tsopano ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulira molimba mtima, komanso atazindikira kuti anali anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anayamba kuwazindikira kuti anali kuyenda ndi Yesu.+

  • Machitidwe 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chotero kwa nthawi yaitali, anakhala akulankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova. Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, mwa kulola kuti zizindikiro ndi zodabwitsa zichitike kudzera mwa ophunzirawo.+

  • 1 Atesalonika 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma mukudziwa kuti choyamba titavutika+ ndi kuchitidwa zachipongwe+ ku Filipi,+ tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula+ kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena