Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kuonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, matemberero otsatirawa adzakugwerani ndi kukupezani:+

  • Yoswa 7:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Tsopano Yoswa ndi Aisiraeli onse anatenga Akani+ mwana wa Zera, limodzi ndi siliva uja, chovala chamtengo wapatali chija, mtanda wa golide uja,+ komanso ana ake aamuna ndi aakazi, ng’ombe zake, abulu, nkhosa, ndiponso hema wake, ndi chilichonse chomwe chinali chake, n’kutsikira nawo kuchigwa cha Akori.+

  • Esitere 9:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Koma Esitere ataonekera pamaso pa mfumu, mfumuyo inalemba lamulo lakuti:+ “Chiwembu+ chake choipa chimene anakonzera Ayuda chimugwere iyeyo.”+ Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+

  • Zekariya 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe m’nyumba ya munthu wakuba ndi m’nyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo m’dzina langa.+ Mpukutuwo upita kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”+

  • Aroma 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+

  • Akolose 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena