27 Tsopano masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, ndi nduna zapamwamba+ za mfumu zimene zinasonkhana zinaonadi kuti motowo sunavulaze amuna amphamvu amenewa,+ ndipo tsitsi lawo silinawauke ndi limodzi lomwe.+ Zovala zawo sizinasinthe ndipo sanali kumveka ngakhale fungo la moto.