10Ku Samariya+ kunali ana aamuna a Ahabu okwanira 70.+ Chotero Yehu analemba makalata n’kuwatumiza kwa atsogoleri+ a ku Yezereeli, kwa akuluakulu,+ ndi kwa anthu amene ankasamalira ana a Ahabu ku Samariya. M’makalatamo analembamo kuti:
21 Rehobowamu anali kukonda kwambiri Maaka mdzukulu wa Abisalomu kuposa akazi ake ena onse+ ndi adzakazi* ake, pakuti iye anakwatira akazi 18, ndiponso anali ndi adzakazi 60. Iye anabereka ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60.