Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 8:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndiyeno Yehova anamva fungo lokhazika mtima pansi,+ moti ananena mumtima+ mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo+ a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.+ Ndipo sindidzawononganso chilichonse monga ndachitiramu.+

  • 1 Mafumu 22:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Yehosafati anayenda m’njira zonse za Asa bambo ake. Sanapatuke panjirazo, ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka. Anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezekawo.+

  • Mlaliki 4:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ine ndinaganiziranso kuponderezana+ konse kumene kukuchitika padziko lapansi pano, ndipo ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa,+ koma panalibe wowatonthoza.+ M’manja mwa oponderezawo munali mphamvu, moti oponderezedwawo analibe wowatonthoza.

  • Danieli 2:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 “M’masiku a mafumu amenewo,+ Mulungu wakumwamba+ adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.+ Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu,+ koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo,+ ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.+

  • Aroma 8:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena