Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iye ndi amene adzamangira dzina langa nyumba,+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+

  • Yesaya 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+

  • Ezekieli 37:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Anthu amenewa adzakhala m’dziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu anakhalamo.+ Adzakhala m’dzikomo+ pamodzi ndi ana awo ndiponso zidzukulu zawo mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wawo mpaka kalekale.+

  • Danieli 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemerero,+ ndi ufumu+ kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+

  • Mika 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+

  • Chivumbulutso 11:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mngelo wa 7 analiza lipenga+ lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake.+ Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena