Danieli 10:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta kufikira milungu itatu yonseyo itatha.+ Mateyu 6:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Koma iwe, pamene ukusala kudya, dzola mafuta m’mutu mwako ndi kusamba nkhope yako,+ Luka 7:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Iwe sunathire mafuta m’mutu mwanga,+ koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira.
3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta kufikira milungu itatu yonseyo itatha.+