Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,+

      Kapena kodi ungadziwe mapeto a kukula kwa Wamphamvuyonse?

  • Yobu 26:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+

      Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.

      Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+

  • Salimo 40:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa,+

      Ndipo mumatiganizira.+

      Palibe angafanane ndi inu.+

      Ndikafuna kulankhula ndi kunena za zodabwitsazo,

      Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

  • Mlaliki 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndinaona ntchito yonse ya Mulungu woona,+ ndipo ndinaona kuti anthu amalephera kudziwa ntchito imene yachitika padziko lapansi pano.+ Kaya anthu ayesetse bwanji kuifufuza, safika poidziwa.+ Ngakhale atanena kuti ali ndi nzeru zokwanira zodziwira zinthu,+ sangathe kuidziwa.+

  • Aroma 11:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena