7 Pamenepo iye adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+ Adzawafunafuna koma sadzawapeza. Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndikufuna kubwerera kwa mwamuna wanga+ woyamba,+ pakuti zinthu zinali kundiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi mmene zilili tsopano.’+