2 Taona! Mdima+ udzaphimba dziko lapansi, ndipo mdima wandiweyani udzaphimba mitundu ya anthu. Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe, ndipo ulemerero wake udzaonekera pa iwe.+
4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu.