1 Mafumu 10:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide,+ siliva, minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko. Ezekieli 27:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 “‘“Zombo za ku Tarisi+ zoyenda m’gulu limodzi zinali kunyamula katundu wako wamalonda. Choncho unalemera ndi kukhala waulemerero kwambiri pakati pa nyanja.+
22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide,+ siliva, minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.
25 “‘“Zombo za ku Tarisi+ zoyenda m’gulu limodzi zinali kunyamula katundu wako wamalonda. Choncho unalemera ndi kukhala waulemerero kwambiri pakati pa nyanja.+