Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Salimo 106:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+

      Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+

      Kuti titamande dzina lanu loyera,+

      Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+

  • Yesaya 66:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ monga mphatso kwa Yehova.+ Adzayenda pamahatchi, pangolo, pangolo zotseka pamwamba, panyulu,* ndi pangamila zazikazi zothamanga,+ popita kuphiri langa loyera,+ ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene ana a Isiraeli amabweretsera mphatso m’nyumba ya Yehova, ataiika m’chiwiya choyera,”+ watero Yehova.

  • Ezekieli 36:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 ‘Ndidzakutengani pakati pa anthu a mitundu ina n’kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko onse. Kenako ndidzakubweretsani m’dziko lanu.+

  • Mika 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.+ Ndidzasonkhanitsa otsala a Isiraeli.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola, komanso ngati gulu la ziweto limene lili pamalo amsipu.+ Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+

  • Zekariya 8:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko la kum’mawa ndiponso kuchokera kudziko la kumadzulo.+

  • Aroma 11:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena