Ekisodo 14:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+ Nehemiya 9:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+ Salimo 78:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,+Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma.+
21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+
11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+