22 Ine ndidzamuweruza+ ndi mliri+ ndiponso magazi.+ Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala,+ moto+ ndi sulufule. Ndidzagwetsa zimenezi pa iyeyo, pagulu lake la asilikali ndi pa mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.+
8 Pambuyo popatsidwa ulemerero,+ Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene anali kukulandani zinthu zanu,+ pakuti Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani,+ akukhudza mwana wa diso langa.+