Deuteronomo
2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,+
Mawu anga adzatsika ngati mame,+
Ngati mvula yowaza pa udzu,+
Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.+
4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+
Njira zake zonse ndi zolungama.+
Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita chosalungama.+
Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+
5 Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa,+
Si ana ake, chilemacho n’chawo.+
Iwo ndiwo m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota!+
6 Kodi mukupitiriza kuchitira Yehova mwa njira imeneyi,+
Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+
Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+
Amene anakupangani ndi kukuchititsani kukhazikika?+
Ganizirani zaka za mibadwomibadwo ya m’mbuyomu.
Funsa bambo ako ndipo akuuza,+
Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.+
8 Pamene Wam’mwambamwamba anapereka cholowa kwa mitundu,+
Pamene analekanitsa ana a Adamu,+
Anaika malire a anthu+
Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+
10 Anam’peza m’dziko lachipululu,+
M’chipululu chopanda kanthu, molira zilombo zakutchire.+
Pamenepo anayamba kum’zungulira,+ kum’samalira,+
Kum’teteza monga mwana wa diso lake.+
11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera mwamphamvu chisa chake,
Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,+
Mmene chimatambasulira mapiko ake, ndi kutenga anawo,
N’kuwanyamula pamapiko ake,+
12 Yehova yekha anapitiriza kumutsogolera,+
Ndipo panalibe mulungu wachilendo kuwonjezera pa iye.+
13 Anapitiriza kumuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+
Moti anadya zokolola za m’minda.+
Anapitirizanso kumudyetsa uchi wochokera m’thanthwe,+
Ndi mafuta ochokera m’mwala wa nsangalabwi.+
14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ng’ombe ndi mkaka wa nkhosa,+
Pamodzi ndi mafuta a nkhosa.
Anamudyetsa nkhosa zamphongo za ku Basana, mbuzi zamphongo,+
Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa ngati mafuta okuta impso.+
Ndipo anali kumwa magazi a mphesa monga vinyo.+
15 Yesuruni*+ atayamba kunenepa, anayamba kupanduka.+
Iwe wanenepa, wakulupala, wakhuta mopitirira muyezo.+
Pamenepo iye anasiya Mulungu amene anam’panga,+
Ndi kunyoza Thanthwe+ la chipulumutso chake.
16 Anayamba kuputa nsanje+ yake ndi milungu yachilendo.+
Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+
17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+
Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+
Milungu yatsopano yongobwera kumene,+
Imene makolo anu akale sanaidziwe.
18 Munaiwala Thanthwe limene linakuberekani,+
Ndipo munayamba kuiwala Mulungu amene anachititsa kuti mukhalepo kudzera mwa zowawa za pobereka.+
19 Yehova ataona zimenezi anayamba kuwanyoza,+
Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakaziwo anam’sautsa.
20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+
Ndione kuti ziwathera bwanji.
Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+
Ana osakhulupirika.+
21 Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+
Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+
Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+
Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+
22 Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+
Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+
Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+
Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+
24 Adzalefuka ndi njala+ ndi kuwonongeka ndi matenda otentha thupi koopsa,+
Ndi chiwonongeko chowawa.+
Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali,+
Pamodzi ndi njoka zapoizoni za m’fumbi.+
25 Kunja lupanga lidzawasandutsa anamfedwa,+
Ndipo mkati mwa nyumba, mantha adzawasandutsa anamfedwa.+
Zimenezi zidzawaphera anyamata ndi anamwali,+
Mwana woyamwa pamodzi ndi munthu wa imvi.+
27 Ngati ndikanati sindikuopa kusautsidwa ndi mdani,+
Kuti adani awo angamve molakwa,+
Kutinso anganene kuti: “Dzanja lathu lapambana,+
Ndipo si Yehova amene wachita zonsezi.”+
30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,
Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+
N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+
Komanso ngati Yehova atawapereka.
32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,
Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+
Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha,
Ndipo ndi zowawa.+
35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+
Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+
Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+
Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+
36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+
Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+
Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera.
Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake.
37 Pamenepo iye adzati, ‘Ili kuti milungu yawo,+
Thanthwe limene anathawirako,+
38 Milungu imene inali kudya mafuta a nsembe zawo,+
Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+
Ibwere kudzakuthandizani.+
Ikhaletu malo anu obisalamo.+
39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+
Ndipo palibe milungu ina pamodzi ndi ine.+
Ndimapha ndiponso ndimapereka moyo.+
Ndavulaza koopsa,+ ndipo ine ndidzachiritsa,+
Palibe aliyense wonditsomphola m’dzanja langa.+
40 Ndikukweza dzanja langa kumwamba polumbira,+
Ndipo ndikunena kuti: “Pali ine, Mulungu wamoyo wosatha,”+
41 Ndikanoladi lupanga langa lonyezimira,+
Dzanja langa likagwira chiweruzo,+
Ndidzalipsira adani anga,+
Ndipo ndidzabwezera chilango kwa odana nane kwambiri.+
42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,+
Magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa.
Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,+
Pamodzi ndi mitu ya atsogoleri a adani.’+
43 Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake,+
Pakuti adzabwezera magazi a atumiki ake,+
Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+
Nadzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”
44 Pamenepo Mose anabwera ndi kulankhula mawu onse a nyimbo iyi m’makutu mwa anthu onse,+ iye pamodzi ndi Hoseya* mwana wa Nuni.+ 45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46 anapitiriza kuwauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse amene ndikulankhula mokuchenjezani lero,+ ndipo muuze ana anu kuti aonetsetse kuti akuchita zimene mawu onse a chilamulo ichi akunena.+ 47 Pakuti amenewa si mawu opanda pake kwa inu,+ chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.+ Mwa kutsatira mawu amenewa mudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu, mutawoloka Yorodano.”+
48 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49 “Kwera m’phiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili m’dziko la Mowabu, moyang’anana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli kuti likhale lawo.+ 50 Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake. 51 Izi zili choncho chifukwa anthu inu munachita mosakhulupirika kwa ine+ pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, m’chipululu cha Zini. Ndiponso chifukwa chakuti anthu inu simunandilemekeze pakati pa ana a Isiraeli.+ 52 Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli.”+