Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 13:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma anthu a ku Sodomu anali oipa, ndipo anali ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.+

  • Deuteronomo 32:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,

      Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+

      Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha,

      Ndipo ndi zowawa.+

  • Yesaya 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,+ ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo lofanana ndi la Sodomu.+ Iwo sanalibise. Tsoka kwa iwo, chifukwa adzibweretsera mavuto.+

  • Maliro 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira chifukwa cha zolakwa zake, n’chachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+

      Mzinda umenewu unawonongedwa mwadzidzidzi m’kanthawi kochepa, ndipo palibe dzanja limene linauthandiza.+

  • Yuda 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena