Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+

      Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+

      Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+

      Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+

  • Salimo 96:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+

      Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+

  • Yesaya 44:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Anthu inu musachite mantha ndipo musathedwe nzeru.+ Kodi sindinachititse aliyense wa inu kuti amve kuyambira nthawi imeneyo? Kodi sindinakuuzeni zimenezi?+ Inu ndinu mboni zanga.+ Kodi palinso Mulungu kupatulapo ine?+ Ayi, palibe Thanthwe.+ Sindikudziwapo aliyense.’”

  • Yeremiya 16:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Kodi munthu wochokera kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeniyeni.+

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

  • 1 Petulo 3:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma ngakhale mutavutika chifukwa cha chilungamo, mudzakhalabe odala.+ Musaope zimene iwo amaopa,+ ndipo musade nazo nkhawa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena