Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pitani mukayendeyende m’misewu ya mu Yerusalemu kuti mukaone, mukafufuze m’mabwalo ake ndi kudziwa ngati mungapezeke munthu,+ ngati muli aliyense wochita chilungamo,+ kapena aliyense wokhulupirika.+ Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu.

  • Yeremiya 9:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndikanakonda kukhala ndi malo a m’chipululu ogona anthu apaulendo.+ Pamenepo ndikanasiya anthu anga ndi kuwachokera, pakuti onsewo ndi achigololo,+ gulu la anthu ochita zachinyengo.+

  • Danieli 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani.

  • Hoseya 7:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Tsoka kwa iwo+ chifukwa andithawa!+ Adzawonongedwa chifukwa chakuti aphwanya malamulo anga. Ine ndinali kufuna kuwawombola,+ koma iwo alankhula mabodza otsutsana nane.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena