Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Koma ngakhale kuti padzachitika zonsezi, pamene iwo akukhala m’dziko la adani awo, sindidzawakana+ kapena kunyansidwa nawo+ moti n’kuwafafaniziratu, kuphwanya pangano langa+ ndi iwo, chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wawo.

  • Nehemiya 9:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Koma mwachifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya,+ pakuti inu ndinu Mulungu wachisomo+ ndi wachifundo.+

  • Salimo 78:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+

      Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+

      Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.

  • Maliro 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+

  • Ezekieli 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “‘“Maso anga anayamba kuwamvera chisoni kuti ndisawawononge,+ chotero sindinawafafanize m’chipululu.

  • Amosi 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Yehova wanena kuti, ‘Taonani, ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndikuyang’ana ufumu wochimwawo,+ ndipo ndidzaufafaniza panthaka ya dziko lapansi.+ Komabe nyumba ya Yakobo+ sindidzaifafaniza yonse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena