9 “‘Lengezani izi pansanja zokhalamo za ku Asidodi ndi pansanja zokhalamo za m’dziko la Iguputo.+ Munene kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti muukire mapiri a Samariya+ ndipo onani zinthu zambiri zachisokonezo ndi zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo.+
23 Zolembazo zinaneneratu kuti Khristu adzavutika,+ ndipo monga woyamba kuukitsidwa kwa akufa,+ iye adzafalitsa kuwala+ mwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina.”+