Yobu 38:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Kodi malamulo akuthambo ukuwadziwa,+Kapena kodi ulamuliro wake ungauike padziko lapansi? Salimo 74:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu.+Inu munapanga chounikira, munapanga dzuwa.+ Salimo 104:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+ Yeremiya 31:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Yehova ndiye Wopereka dzuwa kuti liziwala masana,+ woikira mwezi malamulo,+ wopereka nyenyezi+ kuti ziziwala usiku,+ amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Wochita zimenezi dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye wanena kuti:
35 Yehova ndiye Wopereka dzuwa kuti liziwala masana,+ woikira mwezi malamulo,+ wopereka nyenyezi+ kuti ziziwala usiku,+ amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite phokoso.+ Wochita zimenezi dzina lake ndi Yehova wa makamu.+ Iye wanena kuti: