Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kuonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi mfundo zake zimene ndikukupatsani lero, matemberero otsatirawa adzakugwerani ndi kukupezani:+

  • Deuteronomo 29:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira dziko limeneli mwa kulibweretsera matemberero onse olembedwa m’buku ili.+

  • Yoswa 23:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu analankhula akwaniritsidwa pa inu,+ momwemonso Yehova adzakwaniritsa pa inu mawu onse oipa, kufikira atakufafanizani kukuchotsani padziko labwinoli, limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

  • 2 Mafumu 23:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Koma Yehova anati: “Yuda+ nayenso ndim’chotsa pamaso panga+ monga mmene ndinachotsera Isiraeli,+ ndipo ndithu ndidzakana ngakhale mzinda wa Yerusalemu umene ndinausankha, ndi nyumba imene ndinanena kuti, ‘Dzina langa lizikhala pamenepo.’”+

  • Yeremiya 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “‘Ndidzawagwetsera masoka a mitundu inayi,’+ watero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga+ ndi zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga.

  • Mika 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena