14 Zitatero, akalonga onse anatumiza Yehudi+ mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusa, kukaitana Baruki+ kuti: “Tenga mpukutu umene wawerenga mokweza pamaso pa anthu onse ndipo ubwere nawo kuno.” Pamenepo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo ndi kupita kwa iwo.+