28 Anthu amene adzathawa lupanga kuchoka ku Iguputo kubwerera kudziko la Yuda adzakhala ochepa.+ Ndipo otsala onse ochokera ku Yuda amene akubwera m’dziko la Iguputo kuti adzakhalemo monga alendo adzadziwa kuti ndi mawu a ndani amene ali oona, mawu anga kapena mawu awo.”’”+