Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iwo adzachita mantha ndiponso manyazi chifukwa chakuti anali kudalira Itiyopiya+ komanso chifukwa chakuti anali kusirira kukongola kwa Iguputo.+

  • Yesaya 30:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 amene akupita ku Iguputo+ osafunsira kwa ine,+ ndiponso amene akupita ku Iguputo kuti akapeze chitetezo kwa Farao ndi kukabisala mumthunzi wa Iguputo.+

  • Yesaya 31:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo.+ Iwo akudalira mahatchi wamba+ ndi kukhulupirira magaleta ankhondo,+ chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.+

  • Yeremiya 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Yehova wanena kuti: “Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+ Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu,+ komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.+

  • Yeremiya 42:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 ndipo mukapitiriza kunena kuti: “Ife tikupita kukakhala ku Iguputo,+ kumene sitidzaona nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga komanso kumene sitidzasowa chakudya, moti tikupita kukakhala kudziko limenelo,”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena