Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 33:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+

      Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+

  • Miyambo 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+

  • Miyambo 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+

  • Mlaliki 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nditaganizanso ndinaona kuti padziko lapansi pano anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano,+ amphamvu sapambana pankhondo,+ anzeru sapeza chakudya,+ omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma,+ ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa,+ chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.+

  • Yesaya 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pakuti ilo ndi tsiku la Yehova wa makamu.+ Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza. Lidzafikiranso aliyense wokwezeka kapena wotsika.+

  • Yesaya 16:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, kuti ndi wonyada kwambiri.+ Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, ndi mkwiyo wake.+ Zolankhula zake zodzitukumula sizidzachitika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena