-
1 Samueli 10:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kuchoka pamenepo upitirize ulendo wako mpaka kukafika kumtengo waukulu wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi amuna atatu akupita ku Beteli+ kukapembedza Mulungu woona. Mmodzi wa iwo akhala atanyamula ana atatu a mbuzi,+ wina atanyamula mitanda yobulungira itatu ya mkate,+ ndipo winayo atanyamula mtsuko waukulu wa vinyo.+
-
-
2 Samueli 16:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Davide atapitirira pang’ono pamwamba pa phiri paja,+ anaona Ziba+ mtumiki wa Mefiboseti+ akubwera kudzakumana naye. Iye anali ndi abulu awiri+ okhala ndi zishalo ndipo abuluwa anali atanyamula mitanda 200 ya mkate,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100,+ zipatso za m’chilimwe* 100+ zouma zoumba pamodzi ndiponso mtsuko waukulu wa vinyo.+
-