33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.
64 “Yehova adzakumwazani mwa anthu a mitundu yonse kuchokera kumalekezero ena a dziko mpaka kumalekezero enanso a dziko.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina imene inuyo kapena makolo anu simunaidziwe, milungu yamtengo ndi milungu yamwala.+
4 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho,+ chifukwa cha zimene Manase, mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+