Miyambo 21:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+ Yesaya 1:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu.+ Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.+ Mumasunga masiku okhala mwezi+ ndi sabata,+ ndipo mumaitanitsa misonkhano.+ Koma ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ pamene mukuchita misonkhano yapadera. Yeremiya 7:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 kenako n’kubwera kudzaima pamaso panga m’nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa+ n’kumanena kuti, ‘Ndithudi tidzapulumutsidwa,’ ngakhale mukuchita zinthu zonyansa zonsezi? Ezekieli 23:39 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 39 Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+
27 Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+
13 Musabweretsenso nsembe zina zaufa zopanda phindu.+ Zofukiza zanu ndikunyansidwa nazo.+ Mumasunga masiku okhala mwezi+ ndi sabata,+ ndipo mumaitanitsa misonkhano.+ Koma ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ pamene mukuchita misonkhano yapadera.
10 kenako n’kubwera kudzaima pamaso panga m’nyumba iyi, imene yatchedwa ndi dzina langa+ n’kumanena kuti, ‘Ndithudi tidzapulumutsidwa,’ ngakhale mukuchita zinthu zonyansa zonsezi?
39 Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+