28 Tsoka kwa chisoti chaulemerero cha zidakwa za ku Efuraimu!+ Chisoticho changokhala ngati nkhata yamaluwa yokongola, imene maluwa ake akufota. Nkhata yamaluwayo yavalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala.