Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Salimo 106:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+

      Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+

      Kuti titamande dzina lanu loyera,+

      Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+

  • Yesaya 11:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu n’kusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumalekezero anayi a dziko lapansi.+

  • Yeremiya 30:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu a m’mahema a Yakobo+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pachiunda chake+ ndipo nsanja yokhalamo idzakhala pamalo ake oyenera.+

  • Hoseya 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pamenepo ana a Yuda ndi ana a Isiraeli adzasonkhanitsidwa pamodzi ndipo adzakhala ogwirizana.+ Iwo adzadziikira mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka m’dzikolo,+ chifukwa tsikuli lidzakhala lofunika kwambiri kwa Yezereeli.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena