Deuteronomo 4:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+ Yoswa 23:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Mawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu analankhula akwaniritsidwa pa inu,+ momwemonso Yehova adzakwaniritsa pa inu mawu onse oipa, kufikira atakufafanizani kukuchotsani padziko labwinoli, limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+
26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+
15 Mawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu analankhula akwaniritsidwa pa inu,+ momwemonso Yehova adzakwaniritsa pa inu mawu onse oipa, kufikira atakufafanizani kukuchotsani padziko labwinoli, limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+