Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ndiye chifukwa chake dzikolo n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha kulakwa kwake. Pamenepo dzikolo lidzataya anthu ake kunja.+

  • Salimo 106:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+

      Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,

      Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+

      Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+

  • Yesaya 24:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo,+ chifukwa alambalala malamulo,+ asintha malamulowo+ ndipo aphwanya pangano limene linayenera kukhalapo mpaka kalekale.+

  • Yeremiya 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “M’kupita kwa nthawi, ndinakulowetsani m’dziko la minda ya zipatso kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino za m’dzikolo,+ koma munalowa m’dziko langa ndi kuliipitsa. Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+

  • Yeremiya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+

      Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+

      Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+

  • Yeremiya 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero ndisanawabwezeretse, ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse+ ndi machimo awo onse chifukwa choipitsa dziko langa.+ Anadzaza cholowa changa ndi mitembo ya zinthu zawo zochititsa mseru ndiponso zinthu zawo zonyansazo.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena