-
Ezekieli 6:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Opulumuka anu akadzagwidwa n’kutengedwa kukakhala pakati pa mitundu ina ya anthu, ndithu adzandikumbukira.+ Adzakumbukira mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha mtima wawo wadama umene unawachititsa kundipandukira.+ Adzakumbukiranso mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha maso awo othamangira mafano awo onyansa pofuna kuchita nawo zadama.+ Iwo adzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zawo, chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+
-
-
Zekariya 12:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Posonyeza kuti ndakomera mtima nyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu, ndidzawapatsa mzimu wanga+ umene udzawalimbikitse kundipempha mochonderera.+ Ndithu iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa,+ ndipo adzamulirira ngati mmene amachitira polirira mwana yekhayo wamwamuna. Adzamulira mowawidwa mtima ngati mmene amachitira polira maliro a mwana wamwamuna woyamba kubadwa.+
-