Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo ndidzalola Farao kuumitsa mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzapezerapo ulemerero mwa kugonjetsa Farao ndi magulu ake onse ankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi momwemo.

  • Yesaya 37:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ tipulumutseni m’manja mwake,+ kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+

  • Ezekieli 36:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

  • Ezekieli 38:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndithu iwe udzabwera ngati mitambo kudzaphimba dzikolo ndi kudzaukira anthu anga Aisiraeli.+ Zimenezi zidzachitika m’masiku otsiriza, ndipo ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa.+ Ndidzachita izi kuti anthu a mitundu ina adzandidziwe pamene ndidzadziyeretse pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.”’+

  • Malaki 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera, dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi.+ Anthu azidzapereka zopereka kapena kuti mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa.+ Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakhala lokwezeka pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena