-
2 Mbiri 7:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ana onse a Isiraeli anali kuonerera pamene moto unali kutsika, ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unaonekera pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, nthawi yomweyo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ ndi kuyamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+
-
-
Ezekieli 40:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 M’lifupi mwa malo owaka miyala am’mbali mwa tinyumba ta zipata munali mofanana ndendende ndi m’litali mwa tinyumbato. Amenewa anali malo owaka miyala a m’munsi.
-