Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 21:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Choncho amuna a mumzinda wake, akulu ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzindawo, anachita zimene Yezebeli anawatuma, mogwirizana ndi zimene iye analemba m’makalata amene anawatumizira.+

  • Salimo 74:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Zizindikiro zathu sitinazione, ndipo palibenso mneneri amene watsala,+

      Pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zikhala choncho mpaka liti.

  • Yeremiya 18:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iwo anapitiriza kunena kuti: “Bwerani anthu inu, timukonzere chiwembu Yeremiya,+ pakuti chilamulo sichidzachoka pakamwa pa ansembe athu.+ Anthu athu anzeru sadzaleka kupereka malangizo ndiponso aneneri athu sadzaleka kulosera.+ Tabwerani, tiyeni timuukire ndi malilime athu+ ndipo tisamvere mawu ake ngakhale pang’ono.”

  • Maliro 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Zipata+ zake zamira munthaka. Wawononga mipiringidzo yake ndipo waithyolathyola.

      Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa mitundu ina.+ Malamulo sakutsatiridwa.+

      Aneneri ake sakuonanso masomphenya ochokera kwa Yehova.+

  • Ezekieli 20:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi amuna inu mwabweradi kudzafunsira kwa ine?+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti inu mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena