-
1 Mafumu 11:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Ndichita zimenezi chifukwa iwo andisiya ine+ n’kuyamba kugwadira Asitoreti+ mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi+ mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu+ mulungu wa ana a Amoni. Sanayende m’njira zanga mwa kuchita choyenera pamaso panga ndi kutsatira malamulo anga ndi zigamulo zanga monga anachitira Davide bambo a Solomo.
-
-
Ezara 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kuyambira masiku a makolo athu+ mpaka lero, takhala m’machimo aakulu kwambiri,+ ndipo chifukwa cha zolakwa zathu, ifeyo, mafumu athu,+ ndi ansembe athu,+ taperekedwa m’manja mwa mafumu a mayiko ena ndi lupanga,+ mwa kutengedwa ukapolo,+ kulandidwa katundu,+ komanso kukhala ndi nkhope zamanyazi+ ngati mmene tilili lero.
-