Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 19:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Dziwani kuti Mulungu mwiniwakeyo ndi amene wandisocheretsa,

      Ndipo wandizunguliza ndi ukonde wake wosakira nyama.+

  • Salimo 66:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mwatilowetsa mu ukonde wosakira nyama,+

      Mwatinyamulitsa katundu wolemera m’chiuno mwathu.

  • Yeremiya 52:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo n’kupita nayo ku Ribila,+ kwa mfumu ya Babulo,+ m’dziko la Hamati,+ kuti mfumu ya Babuloyo ikamuweruze.+

  • Maliro 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Iye watumiza moto m’mafupa+ mwanga kuchokera kumwamba, ndipo wafooketsa fupa lililonse.

      Watchera ukonde+ kuti ukole mapazi anga. Wandibweza kumbuyo.

      Wandisandutsa mkazi wosiyidwa popanda thandizo. Ndikudwala tsiku lonse.+

  • Ezekieli 17:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Ndidzam’ponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo ndi kumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+

  • Ezekieli 19:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Mitundu ya anthu a m’zigawo zonse zozungulira anabwera kudzauukira.+ Anauponyera ukonde+ wawo ndipo mkangowo unagwera m’mbuna zawo.+

  • Ezekieli 32:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzakuphimba ndi ukonde+ wanga pogwiritsa ntchito khamu la anthu ambiri a mitundu ina, ndipo iwo adzakukola ndi khoka langa.+

  • Hoseya 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Imvani inu ansembe+ ndipo mvetserani inu a m’nyumba ya Isiraeli. Inunso a m’nyumba ya mfumu+ mvetserani, pakuti chiweruzochi chikukhudza inuyo, chifukwa mwakhala msampha+ ku Mizipa ndipo mwakhala ngati ukonde paphiri la Tabori.+

  • Hoseya 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Kulikonse kumene iwo angapite, ndidzawatchera ndi ukonde.+ Ndidzawagwira ngati zolengedwa zouluka m’mlengalenga.+ Ndidzawalanga mogwirizana ndi chenjezo limene ndinauza msonkhano wawo.+

  • Luka 21:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 ngati msampha.+ Pakuti lidzafikira onse okhala pankhope ya dziko lonse lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena