Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Chotero Yehova anati: “Kudandaula kokhumudwa chifukwa cha Sodomu ndi Gomora+ kwamveka kwambiri, ndipo tchimo lawo n’lalikulu kwambiri.+

  • Nehemiya 9:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Inu ndinu wolungama+ pa zinthu zonse zimene zatichitikira, pakuti inu mwachita zinthu mokhulupirika+ koma ife tachita zinthu zoipa.+

  • Yeremiya 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo adzanena kuti: “Anauchitira zimenezi chifukwa chakuti anthu a mumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo+ ndi kuyamba kulambira milungu ina ndi kuitumikira.”’+

  • Ezekieli 8:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zonyansa kwambiri zimene anthuwa akuchita?+ Ukuona kodi zinthu zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akundichitira kunoko kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zonyansa kwambiri.”

  • Ezekieli 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+

  • Danieli 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.+

  • Aroma 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena