Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Aiguputo+ anenerenji kuti, ‘Anawatulutsa m’dziko lino kuti akawaphe kumapiri ndi kuwafafaniza padziko lapansi’?+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo,+ ndipo mverani chisoni+ anthu anu kuti musawagwetsere tsoka.

  • Numeri 14:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma Mose anamuyankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene munalanditsako anthuwa mwa mphamvu zanu, adzamva ndithu zimenezi.+

  • Deuteronomo 9:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 kuopera kuti anthu a m’dziko+ limene munatitulutsamo anganene kuti: “Chifukwa Yehova sanathe kuwalowetsa m’dziko limene anawalonjeza, komanso chifukwa chakuti anali kudana nawo, anawatulutsa kuti akawaphere m’chipululu.”+

  • Yoswa 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Akanani ndi anthu onse a m’dziko lino adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndithu, ndi kufafaniza dzina lathu kulichotsa padziko lapansi.+ Nanga zikatero mudzaliteteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+

  • 1 Samueli 12:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya+ anthu ake, pakuti Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena