13 “Koma iwe uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti muzisunga masiku anga a sabata,+ pakuti ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu m’mibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.+
2 Muzigwira ntchito masiku 6,+ koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse. Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+